Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 5:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Namani kazembe wa khamu la nkhondo la mfumu ya Aramu anali munthu womveka pamaso pa mbuyace, ndi waulemu; popeza mwa iye Yehova adapulumutsa Aaramu; ndiyenso ngwazi, koma wakhate.

2. Ndipo Aaramu adaturuka magulu magulu, nabwera nalo m'ndende buthu locokera ku dziko la Israyeli, natumikira mkazi wa Namani iyeyu,

3. Nati uyu kwa mbuyace wamkazi, Mbuye wanga akadakhala kwa mneneri ali m'Samariya, akadamciritsa khate lace.

4. Ndipo analowa wina, nauza mbuye wace, kuti, Buthulo lofuma ku dziko la Israyeli lanena zakuti zakuti.

5. Pamenepo mfumu ya Aramu inati, Tiye, muka, ndidzatumiza kalata kwa mfumu ya Israyeli. Pamenepo anacoka, atatenga siliva: matalente khumi, ndi golidi masekeli zikwi zisanu ndi cimodzi, ndi zobvala zakusintha khumi.

6. Ndipo anafika kwa mfumu ya Israyeli ndi kalata, wakuti, Pakulandira kalata uyu, taonani, ndatumiza Namani mnyamata wanga kwa inu, kuti mumciritse khate lace.

7. Ndipo kunali atawerenga kalatayu mfumu ya Israyeli, anang'amba zobvala zace, nati, Ngati ndine Mulungu, kupha ndi kubwezera moyo, kuti ameneyo atumiza kwa ine kumciritsa munthu khate lace? pakuti dziwani, nimupenye, kuti alikufuna cifukwa pa ine.

8. Koma kunali, pamene Elisa munthu wa Mulungu anamva kuti mfumu ya Israyeli adang'amba zobvala zace, anatumiza mau kwa mfumu, ndi kuti, Mwang'amba zobvala zanu cifukwa ninji? Adzetu kwa ine, ndipo adzadziwa kuti muli mneneri m'Israyeli.

9. M'mwemo: Namani anadza ndi akavalo ace ndi magareta ace, naima pakhomo pa nyumba ya Elisa.

10. Ndipo Elisa anamtumira mthenga, ndi kuti, Kasambe m'Yordano kasanu ndi kawiri, ndi mnofu wako udzabwerera momwe, nudzakhala wokonzeka.

11. Koma Namani adapsa mtima, nacoka, nati, Taona, ndinati m'mtima mwanga, kuturuka adzanditurukira, nadzaima ndi kuitana pa dzina la Yehova Mulungu wace, ndi kuweyula dzanja lace pamalopo, ndi kuciritsa wakhateyo.

12. Nanga Abana ndi Faripara, mitsinje ya Damasiko, siiposa kodi madzi onse a m'Israyeli? ndilekerenji kukasamba m'mwemo, ndi kukonzeka? Natembenuka, nacoka morunda.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 5