Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 4:36-44 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

36. Pamenepo anaitana Gehazi, nati, Kaitane Msunemu uja, Namuitana. Ndipo atalowa kuli iye, anati, Nyamula mwana wako.

37. Iye nalowa, nagwa pa mapazi ace, nadziweramitsa pansi; nanyamula mwana wace, naturuka.

38. Ndipo Elisa anabwera ku Giligala, koma m'dzikomo munali njala; ndi ana a aneneri anali kukhala pansi pamaso pace; ndipo anati kwa mnyamata wace, Ika nkhali yaikuruyo, uphikire ana a aneneri.

39. Naturuka wina kukachera ndiwo kuthengo, napeza conga ngati mpesa, nacherapo zipuzi kudzaza m'pfunga mwace, nadza, nazicekera-cekera m'nkhali ya cakudya, popeza sanazidziwa.

40. Pamenepo anagawira anthu kuti adye. Koma kunali; pakudya cakudyaco, anapfuula nati, Munthu wa Mulungu, muli imfa m'nkhalimo. Ndipo sanatha kudyako.

41. Pamenepo anati, Bwera naoni ufa. Nathira m'nkhalimo; nati, Gawirani anthu kuti adye. Ndipo m'nkhalimo munalibe cowawa.

42. Ndipo anadza munthu kucokera ku Baala Salisa, nabwera nayo mikate ya zipatso zoyamba kwa munthu wa Mulungu, mikate ya barele makumi awiri, ndi ngala zaziwisi za tirigu zosaomba. Ndipo anati, Uwapatse anthu kuti adye.

43. Koma mnyamata wace anati, Ciani? ndigawire amuna zana ici kodi? Koma anati, Uwapatse anthu kuti adye; pakuti atero Yehova, Adzadya nadzasivako.

44. Potero anawagawira, nadya, nasiyapo, monga mwa mau a Yehova.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 4