Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 4:25-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Potero anamuka, nafika kwa munthu wa Mulungu ku phiri la Karimeli. Ndipo kunali, pakumuona munthu wa Mulungu alinkudza kutali, anati kwa Gehazi mnyamata wace, Tapenya, suyo Msunemu uja;

26. uthamange tsopano kukomana naye, nunene naye, Muli bwino kodi? mwamuna wanu ali bwino? mwanayo ali bwino? Ndipo anati, Ali bwino.

27. Ndipo pofika kwa munthu wa Mulungu kuphiri anamgwira mapazi. Ndipo Gehazi anayandikira kuti amkankhe; koma munthu wa Mulungu anati, Umleke, pakuti mtima wace ulikumwawa; ndipo Yehova wandibisira osandiuza ici.

28. Ndipo mkaziyo anati, Ngati ndinapempha mwana kwa mbuyanga? Kodi sindinati, Musandinyenga?

29. Pamenepo anati kwa Gehazi, Udzimangire m'cuuno, nutenge ndodo yanga m'dzanja lako, numuke; ukakomana ndi munthu usamlankhule; akakulankhula wina usamyankhe; ukaike ndodo yanga pankhope pa mwanayo.

30. Koma mace wa mwana anati, Pali Yehova, pali inunso, ngati nkukusiyani. Ndipo ananyamuka, namtsata.

31. Nawatsogolera Gehazi, naika ndodo pankhope pa mwanayo; koma mwanayo analibe mau, kapena kusamalira. Motero anabwerera kukomana naye, namuuza kuti, Sanauke mwanayo.

32. Ndipo pamene Elisa analowa m'nyumba, taonani, mwanayo ngwakufa, adamgoneka pakama pace.

33. Nalowa Elisa, nadzitsekera awiriwa, napemphera kwa Yehova.

34. Nakwera, nagona pa mwanayo ndi kulinganiza pakamwa pace ndi pakamwa pace, maso ace ndi maso ace, zikhato zace ndi zikhato zace, nadzitambasula pa iye, ndi mnofu wa mwana unafunda.

35. Pamenepo anabwera nayenda m'nyumba, cakuno kamodzi, cauko kamodzi; nakwera, nadzitambasuliranso pa iye; ndi mwana anayetsemula kasanu ndi kawiri, natsegula mwanayo maso ace.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 4