Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 23:8-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Naturutsa ansembe onse m'midzi ya Yuda, nawaipitsira misanje, imene ansembe adafukizapo zonunkhira, kuyambira Geba kufikira Beereseba; napasula misanje ya kuzipata, yokhala polowera pa cipata ca Yoswa kazembe wa mudzi, yokhala ku dzanja lako lamanzere kwa cipata ca mudzi.

9. Koma ansembe a misanje sanakwera kudza ku guwa la nsembe la Yehova ku Yerusalemu; koma anadya mkate wopanda cotupitsa pakati pa abale ao.

10. Anawaipitsiranso Tofeti, wokhala m'cigwa ca ana a Hinomu; kuti asapitirize mmodzi yense mwana wace wamwamuna kapena wamkazi pamoto kwa Moleki.

11. Nacotsanso akavalo amene mafumu a Yuda adapereka kwa dzuwa, polowera nyumba ya Yehova, ku cipinda ca Natani Meleki mdindoyo, cokhala kukhonde; natentha magareta a dzuwa ndi moto.

12. Ndi maguwa a nsembe anali patsindwi pa cipinda cosanja ca Ahazi adawapanga mafumu a Yuda, ndi maguwa a nsembe adawapanga Manase m'mabwalo awiri a nyumba ya Yehova, mfumu inawagumula, niwacotsa komweko, nitaya pfumbi lao ku mtsinje wa Kidroni.

13. Ndipo mfumu inawaipitsira misanje yokhala kum'mawa kwa Yerusalemu, ndiyo ya ku dzanja lamanja la phiri la cionongeko, imene Solomo mfumu ya Israyeli adaimangira Asitoreti conyansa ca Asidoni, ndi Kemosi conyansa ca Moabu, ndi Milikomu conyansa ca ana a Amoni.

14. Nathyolathyola zoimiritsa, nalikha zifanizo, nadzaza pamalo pao ndi mafupa a anthu.

15. Anagumulanso guwa la nsembe linali ku Beteli, ndi msanje adaumanga Yerobiamu mwana wa Nebati wolakwitsa Israyeli uja; guwa la nsembelo, ndi msanje womwe anagumula; natentha msanje, naupondereza ukhale pfumbi, natentha cifanizoco.

16. Ndipo potembenuka Yosiya anaona manda okhalako kuphiri, natumiza anthu naturutsa mafupa kumanda, nawatentha pa guwa la nsembe, kuliipitsa, monga mwa mau a Yehova anawalalikira munthu wa Mulungu wolalikira izi.

17. Anatinso, Cizindikilo ici ndiciona nciani? Namuuza anthu a m'mudziwo, Ndico manda a munthu wa Mulungu anafuma ku Yuda, nalalikira izi mwazicitira guwa la nsembe la ku Beteli.

18. Nati iye, Mlekeni, munthu asakhudze mafupa ace. Naleka iwo mafupa ace akhale pamodzi ndi mafupa a mneneri uja anaturuka m'Samariya.

19. Ndi nyumba zonse zoo mwe za ku misanje yokhala m'midzi ya Samariya, adazimanga mafumu a Israyeli kuutsa nazo mkwiyo wa Yehova, Yosiya anazicotsa, nazicitira monga mwa nchito zonse adazicita ku Beteli.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 23