Anatinso, Cizindikilo ici ndiciona nciani? Namuuza anthu a m'mudziwo, Ndico manda a munthu wa Mulungu anafuma ku Yuda, nalalikira izi mwazicitira guwa la nsembe la ku Beteli.