Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 2:14-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Ndipo anatenga copfunda ca Eliya cidamtayikiraco, napanda madziwo, nati, Ali kuti Yehova Mulungu wa Eliya? Ndipo atapanda madziwo anagawikana kwina ndi kwina, naoloka Elisa.

15. Ndipo pamene anampenya ana a aneneri okhala ku Yeriko pandunji pace, anati, Mzimu wa Eliya watera pa Elisa. Ndipo anadza kukomana naye, nadziweramitsa pansi kumaso kwace.

16. Ndipo ananena naye, Taonani, tsono anyamata anufe tiri nao amuna makumi asanu amphamvu, amuke kukafuna mbuye wanu; kapena wamkweza mzimu wa Yehova ndi kumponya pa phiri lina, kapena m'cigwa dna. Koma anati, Musatumiza.

17. Koma anamuumiriza kufikira anacita manyazi; pamenepo anati, Tumizani. Motero anatumiza amuna makumi asanu, namfunafuna iwo masiku atatu, osampeza.

18. Nabwerera kwa iye ali cikhalire ku Yeriko, ndipo anati kwa iwo, Kodi sindinanena nanu, Musamuka?

19. Ndipo amuna a kumudzi anati kwa Elisa, Taonani, pamudzi pano mpabwino, monga umo aonera mbuye wanga; koma madzi ndi oipa, ndi nthaka siibalitsa.

20. Pamenepo anati, Nditengereni cotengera catsopano, muikemo mcere. Ndipo anabwera naco kwa iye.

21. Ndipo anaturuka kumka ku magwero a madzi, nathiramo mcere, nati, Atero Yehova, Ndaciritsa madzi awa, sikudzafumirakonso imfa, kapena kusabalitsa.

22. Cotero madzi anaciritsidwa mpaka lero lino, monga mwa mau a Elisa ananenawo.

23. Ndipo anacokako kukwera ku Beteli, ndipo iye ali cikwerere m'njiramo, munaturuka anyamata ang'ono m'mudzimo, namseka, nati kwa iye, Takwera wadazi, takwera wadazi!

24. Ndipo anaceuka, nawaona, nawatemberera m'dzina la Yehova. Ndipo kuthengo kunaturuka zimbalangondo ziwiri zazikazi, ndi kupwetedza mwa iwo ana makumi anai mphambu awiri.

25. Ndipo anacokako kumka ku phiri la Karimeh; nabwera kumeneko nafika ku Samariya.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 2