Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 19:6-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Nanena nao Yesaya, Muzitero kwa mbuye wanu, Atero Yehova, Musamaopa mau mudawamva, amene anyamata a mfumu ya Asuri anandicitira nao mwano.

7. Taonani, ndidzalonga mwa iye mzimu wakuti adzamva mbiri, nadzabwerera kumka ku dziko lace, ndipo ndidzamgwetsa ndi lupanga m'dziko lace.

8. Nabwerera kazembeyo, napeza mfumu ya Asuri alikuthira nkhondo pa Libina, popeza anamva kuti adacoka ku Lakisi.

9. Ndipo anamva za Tirihaka mfumu ya Kusi, akuti, Taonani, waturuka kuthirana nawe nkhondo. Pamenepo anatumizanso mithenga kwa Hezekiya, ndi kuti,

10. Muzitero naye Hezekiya mfumu ya Yuda, kuti, Asakunyenge Mulungu wako amene umkhulupirira, ndi kuti, Yerusalemu sudzaperekedwa m'dzanja la mfumu ya Asuri.

11. Taona, udamva ico mafumu a Asuri anacitira maiko onse, ndi kuwaononga konse; ndipo uti upulumuke ndiwe kodi?

12. Kodi milunguyaamitundu inawalanditsa amene makolo anga anawaononga, ndiwo Gozani, ndi Hara Rezefi, ndi ana a Edeni okhala m'Telasara?

13. Iri kuti mfumu ya Hamati, ndi mfumu ya Aripadi, ndi mfumu ya mudzi wa Sefaravaimu, wa Hena, ndi Iva?

14. Ndipo Hezekiya analandira kalatayo ku dzanja la mithenga, namwerenga, nakwera Hezekiya kumka ku nyumba ya Yehova, namfunyulula pamaso pa Yehova.

15. Napemphera Hezekiya pamaso pa Yehova, nati, Yehova Mulungu wa Israyeli wakukhala pakati pa akerubi, Inu ndinu Mulungu mwini wace, Inu nokha, wa maufumu onse a dziko lapansi; munalenga kumwamba ndi dziko lapansi.

16. Cherani khutu lanu, Yehova, nimumve; tsegulani maso anu, Yehova, nimupenye; ndipo imvani mau a Sanakeribu, amene anatumiza kutonza nao Mulungu wamoyo.

17. Zoona, Yehova, mafumu a Asuri anapasula amitundu ndi maiko ao,

18. naponya milungu yao kumoto; popeza sindiyo milungu koma yopanga anthu ndi manja ao, mtengo ndi mwala; cifukwa cace anaiononga.

19. Ndipo tsono, Yehova Mulungu wathu, mutipulumutse m'dzanja lace, kuti adziwe maufumu onse a dziko lapansi kuti Inu ndinu Yehova Mulungu, Inu nokha nokha.

20. Pamenepo Yesaya mwana wa Amozi anatumiza kwa Hezekiya, ndi, kuti, Atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Condipempha iwe pa Sanakeribu mfumu ya Asuri ndacimva.

21. Mau a Yehova akumnenera iye ndi awa, Namwali mwana wamkazi wa Ziyoni akunyoza, akuseka mwana wamkazi wa Yerusalemu, akupukusira mutu pambuyo pako.

22. Ndiye yani wamtonza ndi kumcitira mwano? ndiye yani wamkwezera mau ndi kumgadamira maso ako m'mwamba? Ndiye Woyerayo wa Israyeli.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 19