Napemphera Hezekiya pamaso pa Yehova, nati, Yehova Mulungu wa Israyeli wakukhala pakati pa akerubi, Inu ndinu Mulungu mwini wace, Inu nokha, wa maufumu onse a dziko lapansi; munalenga kumwamba ndi dziko lapansi.