Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 19:16-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Cherani khutu lanu, Yehova, nimumve; tsegulani maso anu, Yehova, nimupenye; ndipo imvani mau a Sanakeribu, amene anatumiza kutonza nao Mulungu wamoyo.

17. Zoona, Yehova, mafumu a Asuri anapasula amitundu ndi maiko ao,

18. naponya milungu yao kumoto; popeza sindiyo milungu koma yopanga anthu ndi manja ao, mtengo ndi mwala; cifukwa cace anaiononga.

19. Ndipo tsono, Yehova Mulungu wathu, mutipulumutse m'dzanja lace, kuti adziwe maufumu onse a dziko lapansi kuti Inu ndinu Yehova Mulungu, Inu nokha nokha.

20. Pamenepo Yesaya mwana wa Amozi anatumiza kwa Hezekiya, ndi, kuti, Atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Condipempha iwe pa Sanakeribu mfumu ya Asuri ndacimva.

21. Mau a Yehova akumnenera iye ndi awa, Namwali mwana wamkazi wa Ziyoni akunyoza, akuseka mwana wamkazi wa Yerusalemu, akupukusira mutu pambuyo pako.

22. Ndiye yani wamtonza ndi kumcitira mwano? ndiye yani wamkwezera mau ndi kumgadamira maso ako m'mwamba? Ndiye Woyerayo wa Israyeli.

23. Watonza Yehova mwa mithenga yako, nuti, Ndi magareta anga aunyinji ndakwera pa misanje ya mapiri ku mbali zace za Lebano, ndipo ndidzagwetsa mikungudza yace yaitali, ndi mitengo yace yosankhika yar mlombwa, ndidzalowanso m'ngaka mwace mweni mweni, ku nkhalango zace za madimba.

24. Ndakapa, ndamwa madzi acilendo, ndi ku mapazi anga ndidzaphwetsa mitsinje yonse ya Aigupto,

25. Sunamva kodi kuti Ine ndinacicita kale lomwe, ndi kucipanga masiku akalekale? tsopano ndacifikitsa kuli iwe, uzikhala wakupasula imidzi yamalinga ikhale miunda ya mabwinja.

26. Cifukwa cace okhalamo ao anali ofok a manja, anaopsedwa, nacita manyazi, ananga udzu wa kuthengo, ndi msipu wauwisi, ndi udzu wa patsindwi, ndi tirigu wopserera asanakule.

27. Koma ndidziwa kukhala pansi kwako, ndi kuturuka kwako, ndi kulowa kwako, ndi kundizazira kwako.

28. Cifukwa ca kundizazira kwako, ndi popeza kudzikuza kwako kwandifikira m'makutu mwanga, ndidzakukowa ndi ngowe yanga m'mphuno mwako, ndi cam'kamwa canga m'milomo mwako; ndipo ndidzakubwezera pa njira unadzerayi.

29. Ndi ici ndi cizindikilo cako: caka cino mudzadya za mphulumukwa, ndi caka ca mawa za mankhokwe, ndi caka camkuca muzibzala ndi kukolola, muzioka minda yampesa ndi kudya zipatso zace.

30. Ndipo opulumuka a nyumba ya Yuda otsalawo adzaphukanso mizu, ndi kupatsa zipatso pamwamba.

31. Pakuti ku Yerusalemu kudzaturuka otsala, ndi akupulumukawo ku phiri la Ziyoni; cangu ca Yehova cidzacita ici.

32. Cifukwa cace atero Yehova za mfumu ya Asuri, iye sadzalowa m'mudzi muno, kapena kuponyamo mubvi, kapena kufikako ndi cikopa, kapena kuundira mtumbira.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 19