Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 16:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Caka cakhumi mphambu zisanu ndi ziwiri ca Peka mwana wa Remaliya Ahazi mwana wa Yotamu mfumu ya Yuda analowa ufumu wace.

2. Ahazi anali wa zaka makumi awiri polowa ufumu wace, nakhala mfumu zaka khumi mphambu zisanu ndi cimodzi m'Yerusalemu; koma sanacita zoongoka pamaso pa Yehova Mulungu wace, ngati Davide kholo lace;

3. popeza anayenda m'njira ya mafumu a Israyeli, napititsanso mwana wace pamoto, monga mwa zonyansa za amitundu amene Yehova anawaingitsa pamaso pa ana a Israyeli.

4. Ndipo anaphera nsembe, nafukiza zonunkhira kumisanje, ndi kuzitunda, ndi patsinde pa mtengo uli wonse wogudira.

5. Pamenepo Rezini mfumu ya Aramu, ndi Peka mwana wa Remaliya mfumu ya Israyeli, anakwera kumka ku Yerusalemu kukacita nkhondo, nammangira Ahazi misasa; koma sanakhoza kumgonjetsa.

6. Nthawi yomweyo Rezini mfumu ya Aramu anabwezera Elati kwa Aramu, napitikitsa Ayuda ku Elati; nadza Aaramu ku Elati, nakhala komweko kufikira lero lino.

7. Ndipo Ahazi anatuma mithenga kwa Tigilati Pilesere mfumu ya Asuri, ndi kuti, Ine ndine kapolo wanu ndi mwana wanu; kwerani, mudzandipulumutse m'dzanja la mfumu ya Aramu, ndi m'dzanja la mfumu ya Israyeli anandiukirawo.

8. Natenga Ahazi siliva ndi golidi wopezeka m'nyumba ya Yehova, ndi ku cuma ca nyumba ya mfumu, nazitumiza mtulo kwa mfumu ya Asuri.

9. Nimmvera mfumu ya Asuri, nikwera kumka ku Damasiko mfumu ya Asuri, niulanda, nipita nao anthu ace andende ku Kiri, nimupha Rezini.

10. Ndipo mfumu Ahazi anamuka ku Damasiko kukakomana ndi Tigilati Pilesere mfumu ya Asuri, naona guwa la nsembe linali ku Damasiko; natumiza mfumu Ahazi kwa Uriya wansembe cithunzithunzi cace, ndi cifanizo cace, monga mwa mamangidwe ace onse.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 16