Ndipo mfumu Ahazi anamuka ku Damasiko kukakomana ndi Tigilati Pilesere mfumu ya Asuri, naona guwa la nsembe linali ku Damasiko; natumiza mfumu Ahazi kwa Uriya wansembe cithunzithunzi cace, ndi cifanizo cace, monga mwa mamangidwe ace onse.