Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 15:9-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Nacita iye coipa pamaso pa Yehova, monga adacita makolo ace; sanaleka zolakwa zace za Yerobiamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israyeli.

10. Ndipo Salumu mwana wa Yabesi anamcitira ciwembu, namkantha pamaso pa anthu, namupha; nakhala mfumu m'malo mwace.

11. Macitidwe ena tsono a Zekariya, taonani, zalembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli.

12. Awa ndi mau a Yehova anawanena ndi Yehu, ndi kuti, Ana ako kufikira mbadwo wacinai adzakhala pa mpando wacifumu wa Israyeli. Ndipo kunatero momwemo.

13. Salumu mwana wa Yabesi analowa ufumu wace caka ca makumi atatu mphambu zisanu ndi zinai ca Uziya mfumu ya Yuda, nakhala mfumu mwezi umodzi m'Samariya.

14. Koma anakwera Menahemu mwana wa Gadi kucokera ku Tiriza, nafika ku Samariya, nakantha Salumu mwana wa Yabesi m'Samariya, namupha; nakhala mfumu m'malo mwace.

15. Macitidwe ena tsono a Salumu ndi ciwembu cace anacicita, taonani, zalembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli.

16. Pamenepo Menahemu anakantha Tifisa, ndi onse anali m'mwemo, ndi malire ace kuyambira ku Tiriza; popeza sanamtsegulira pacipata; anaukantha, natumbula akazi onse a pakati okhala m'mwemo.

17. Caka ca makumi atatu mphambu zisanu ndi zinai ca Azariya mfumu ya Yuda, Menahemu mwana wa Gadi analowa ufumu wace wa Israyeti, nakhala mfumu zaka khumi m'Samariya.

18. Nacita coipa pamaso pa Yehova masiku ace onse, osaleka zolakwa za Yerobiamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israyeli.

19. Pamenepo Puli mfumu ya Asuri anadza kudzamenyana ndi dziko, koma Menahemu anampatsa Puli matalente a siliva cikwi cimodzi; kuti dzanja lace likhale naye kukhazikitsa ufumu m'dzanja lace.

20. Ndipo Menahemu anasonkhetsa Israyeli ndaramazi, nasonkhetsa acuma, yense masekeli makumi asanu a siliva: kuti azipereke kwa mfumu ya Asuri. Nabwerera mfumu ya Asuri osakhala m'dzikomo.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 15