Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 9:9-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Kale m'Israyeli, munthu akati afunse kwa Mulungu, adafotero kuti, Tiyeni tipite kwa mlauliyo; popeza iye wochedwa mneneri makono ano, anachedwa mlauli kale.

10. Pamenepo Sauli anati kwa mnyamata wace, Wanena bwino; tiye tipite. Comweco iwowa anapita kumudzi kumene kunali munthu wa Mulunguyo.

11. Pakukwera kumudziko anapeza anthu akazi alikuturuka kuti akatunge madzi, nanena nao, Mlauliyo alipo kodi?

12. Ndipo anawayankha nati, Alipo; onani ali m'tsogolo mwanu; fulumirani pakuti wabwera lero kumudzi kuno; popeza lero anthu akuti aphere nsembe pamsanje;

13. mutafika m'mudzi, pomwepo mudzampeza, asanakwere kumsanje kukadya; pakuti anthu sadzadya, koma iye atafika ndipo; pakuti iye amadalitsa nsembeyo; ndipo atatero oitanidwawo amadya. Cifukwa cace kwerani; popeza nthawi yino mudzampeza.

14. Ndipo iwowa anakwera kumudzi; ndipo m'mene analowa m'mudzimo, onani, Samueli anaturukira pali Iwo, kuti akakwere kumsanje.

15. Ndipo Yehova anaululiratu m'khutu la Samueli dzulo lace la tsiku limene Sauli anabwera, kuti,

16. Mawa, monga dzuwa lino, ndidzakutumizira munthu wocokera ku dziko la Benjamini, udzamdzoza iye akhale mtsogoleri wa anthu anga Israyeli, kuti akawapulumutse anthu anga m'manja a Afilisti; pakuti Ine ndinapenya pa anthu anga, popeza kulira kwao kunandifika Ine.

17. Ndipo pamene Samueli anaona Sauli, Yehova anati kwa iye, Ona munthu amene ndinakuuza za iye! ameneyu adzaweruza anthu anga.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 9