Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 7:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo anthu a ku Kiriati-yearimu anabwera, natenga likasa la Yehova, nafika nalo m'nyumba ya Abinadabu paphiri; napatula mwana wace wamwamuna Eleazeri kuti asunge likasa la Yehova.

2. Ndipo kunali, kuti likasalo linakhala nthawi yaikuru m'Kiriati-yearimu; popeza linakhalako zaka makumi awiri; ndipo banja lonse la Israyeli linalirira Yehova.

3. Ndipo Samueli analankhula ndi banja lonse la Israyeli nati, Ngati mukuti mubwerere kunka kwa Yehova ndi mitima yanu yonse, cotsani pakati pa inu milungu yacilendo, ndi Asitaroti, nimukonzere Yehova mitima yanu, ndi kumtumikira iye yekha; mukatero, iye adzakupulumutsani m'manja a Afilisti.

4. Pomwepo ana a Israyeli anacotsa. Abaala ndi Asitaroti, natumikira Yehova yekha.

5. Ndipo Samueli anati, Musonkhanitse Aisrayeli onse ku Mizipa, ndipo ine ndidzakupemphererani kwa Yehova.

6. Ndipo anaunjikana ku Mizipa, natunga madzi, nawatsanula pamaso pa Yehova, nasala cakudya tsiku lija, nati, Tinacimwira Yehova. Ndipo Samueli anaweruza ana a Israyeli m'Mizipa.

7. Ndipo pamene Afilisti anamva kuti Aisrayeli anasonkhana pamodzi ku Mizipa, mafumu a Afilisti anakwera kukayambana ndi Aisrayeli. Ndipo Aisrayeli pakumva ici, anacita mantha ndi Afilistiwo.

8. Ndipo ana a Israyeli anati kwa Samueli, Musaleke kutipempherera kwa Yehova Mulungu wathu, kuti iye atipulumutse m'manja a Afilistiwo.

9. Ndipo Samueli anatenga mwana wa nkhosa woyamwa, nampereka wathunthu kwa Yehova, nsembe yopsereza; ndipo Samueli anapempherera Israyeli kwa Yehova; ndipo Yehova anambvomereza.

10. Ndipo pamene Samueli analikupereka nsembe yopserezayo, Afilisti anayandikira kuti aponyane ndi Aisrayeli; koma tsiku lomwe lija Yehova anagunda ndi kugunda kwakukuru pa Afilistiwo, nawapolonganitsa. Ndipo anakanthidwa pamaso pa Aisrayeli.

11. Ndipo Aisrayeli anaturuka ku Mizipa, nathamangira Afilisti, nawakantha mpaka anafika pansi pa Betikara.

12. Pamenepo Samueli anatenga mwala nauimika pakati pa Mizipa ndi Seni, naucha dzina lace. Ebenezeri, nati, Kufikira pano Yehovaanatithandiza.

13. Comweco anagonjetsa Afilisti, ndino iwo sanatumphanso malire a Israyeli ndipo dzanja la Yehova linasautsa Afilisti masiku onse a Samueli.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 7