Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 6:12-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo ng'ombezo zinatsata njira yolunjika ku Betisemesi, niziyenda mumseu, zirikulira poyenda; sizinapambukira ku dzanja lamanja, kapena kulamanzere; ndipo mafumu a Afilisti anazitsatira kufikira ku malire a Betisemesi.

13. Ndipo a ku Betisemesi analikumweta tirigu wao m'cigwamo; natukula maso ao, naona likasalo, nakondwerapakuliona.

14. Ndipo garetalo linafika m'munda wa Yoswa wa ku Betisemesi, ndi kuima momwemo, pa mwala waukuru; ndipo anawaza matabwa a garetalo, nazipereka ng'ombezo nsembe yopsereza kwa Yehova.

15. Ndipo Alevi anatsitsa likasa la Yehova, ndi bokosi linali nalo, m'mene munali zokometsera zagolidi, naziika pa mwala waukuruwo; ndipo anthu a ku Betisemesi anapereka nsembe zopsereza, naphera nsembe kwa Yehova tsiku lomwelo.

16. Ndipo pamene mafumu asanu a Afilisti anaonerako, anabwerera kunka ku Ekroni tsiku lomwelo.

17. Ndipo amenewa ndiwo mafundo agolidi amene anabwezera kwa Yehova akhale nsembe yoparamula, kwa Asidodi limodzi, kwa Gaza limodzi, kwa Asikeloni limodzi, kwa Gati limodzi, kwa Ekroni limodzi;

18. ndiponso mbewa zagolidi, monga ciwerengo ca midzi yonse ya mafumu asanu a Afilisti, midzi ya malinga, ndi midzi ya kumiraga; kufikira ku mwala waukuru, adaikapo likasa la Yehova; mwalawo ulipobe kufikira lero m'munda wa Yoswa wa ku Betisemesi.

19. Ndipo Mulungu anakantha anthu a ku Betisemesi, cifukwa anasuzumira m'likasa la Yehova, anakantha anthu zikwi makumi asanu; ndipo anthu analira maliro, cifukwa Yehova anawakantha anthuwo ndi makanthidwe akuru.

20. Ndipo a ku Betisemesi anati, Akhoza ndani kuima pamaso pa Yehova, Mulungu Woyera uyu? Ndipo adzakwera kwa yani pakuticokera ife?

21. Ndipo anatumiza mithenga kwa anthu a ku Kiriati-yearimu, nati, Afilisti anabwera nalo likasa la Yehova, mutsike; ndi kukwera nalo kwanu.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 6