Ndipo ng'ombezo zinatsata njira yolunjika ku Betisemesi, niziyenda mumseu, zirikulira poyenda; sizinapambukira ku dzanja lamanja, kapena kulamanzere; ndipo mafumu a Afilisti anazitsatira kufikira ku malire a Betisemesi.