Ndipo garetalo linafika m'munda wa Yoswa wa ku Betisemesi, ndi kuima momwemo, pa mwala waukuru; ndipo anawaza matabwa a garetalo, nazipereka ng'ombezo nsembe yopsereza kwa Yehova.