Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 5:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Afilisti anatenga likasa la Mulungu, nacoka nalo ku Ebenezeri, napita ku Asidodi.

2. Ndipo Afilistiwo anatenga likasa la Mulungu, nafika nalo ku nyumba ya Dagoni, naliika pafupi ndi Dagoni.

3. Ndipo pakuuka a ku Asidodi mamawa, taonani Dagoni adagwa pansi, nagona cafufumimba patsogolo pa likasa la Yehova. Ndipo iwo anatenga Dagoni namuimikanso m'malo mwace.

4. Ndipo m'mawa mwace polawirira, taonani, Dagoni adagwa pansi, nagona cafufumimba patsogolo pa likasa la Yehova; ndipo mutu wace ndi zikhato zonse ziwiri za manja ace zinagona zoduka paciundo; Dagoni anatsala thupi lokha.

5. Cifukwa cace angakhale ansembe, angakhale ena akulowa m'nyumba ya Dagoni, palibe woponda pa ciundo ca Dagoni ku Asidodi, kufikira lero lino.

6. Koma Yehova anabvuta iwo a ku Asidodi ndi dzanja lace, nawaononga, nawazunza ndi mafundo, m'Asidodi ndi m'miraga yace.

7. Ndipo pamene anthu a ku Asidodi anaona kuti ncomweco, anati iwowa, Likasa la Mulungu wa Israyeli lisakhalitse ndi ife; popeza dzanja lace litiwawira ife, ndi Dagoni mulungu wathu.

8. Cifukwa cace anatumiza mithenga, nasonkhanitsa mafumu onse a Afilisti, nati, Ticite nalo ciani likasa la Mulungu wa Israyeli? Ndipo anati, Anyamule likasa la Mulungu kunka nalo ku Gati, Ndipo ananyamula likasalo la Mulungu wa Israyeli, napita nalo kumeneko.

9. Ndipo kunali atafika nalo, dzanja la Yehova linatsutsa mudziwo ndi kusautsa kwakukuru; ndipo anazunza anthu a mudziwo, akuru ndi ang'ono; ndi mafundo anawabuka.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 5