Ndipo kunali atafika nalo, dzanja la Yehova linatsutsa mudziwo ndi kusautsa kwakukuru; ndipo anazunza anthu a mudziwo, akuru ndi ang'ono; ndi mafundo anawabuka.