Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 4:6-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo Afilistiwo pakumva kubuma pa kupfuula kwao, anati, Phokoso ili la kupfuula kwakukuru ku zithando za Aisrayeli litani? Ndipo anamva kuti likasa la Yehova lidzafika ku zithandozo.

7. Ndipo Afilisti anaopa, pakuti anati, Mulungu wafika kuzithando. Ndipo iwo anati, Tsoka kwa ife! popeza kale lonse panalibe cinthu cotere.

8. Tsoka kwa ife! adzatilanditsa ndani m'manja a milungu yamphamvu imeneyi? Milungu ija inakantha Aaigupto ndi masautso onse m'cipululu ndi yomweyi.

9. Limbikani, ndipo mucite camuna, Afilisti inu, kuti mungakhale akapolo a Ahebri, monga iwowa anali akapolo anu. Citani camuna nimuponyane nao.

10. Ndipo Afilisti anaponyana nao, nakantha Aisrayeli; iwowa nathawira, munthu yense ku hema wace; ndipo kunali kuwapha kwakukuru; popeza anafako Aisrayeli zikwi makumi atatu a oyenda pansi.

11. Ndipo likasa la Mulungu linalandidwa, ndi ana awiri a Eli, Hofeni ndi Pinehasi, anaphedwa.

12. Ndipo munthu wa pfuko la Benjamini anathamanga kucokera ku khamu la ankhondo, nafika ku Silo tsiku lomwelo, ndi zobvala zace zong'ambika, ndi dothi pamutu pace.

13. Pakufika iye, onani, Eli analikukhala pampando m'mbali mwa njira, alikuyang'anira, popeza mtima wace unanthunthumira cifukwa ca likasa la Mulungu, Pamene munthu uja anafika m'mudzimo, nanena izi, a m'mudzi monse analira.

14. Ndipo Eli, pakumva kubuma kwa kulira kwao, anati, Alikupokoseranji? Ndipo munthuyo anafulumira, nadza nauza Eli.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 4