Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 3:8-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndipo Yehova anabwereza kumuitana Samueli nthawi yacitatu. Ndipo iye anauka napita kwa Eli, nati, Ndine, pakuti mwandiitana ndithu. Ndipo Eli anazindikira kuti ndiye Yehova amene analikuitana mwanayo.

9. Cifukwa cace Eli anati kwa Samueli, Pita, ukagone; ndipo akakuitananso, ukabvomere, kuti, Nenani, Yehova, popeza mnyamata wanu akumva. Comweco Samueli anakagona m'malo mwace.

10. Ndipo Yehova anabwera, naimapo, namuitana monga momwemo, Samueli, Samueli. Pompo Samueli anayankha, Nenani, popeza mnyamata wanu akumva.

11. Ndipo Yehova ananena ndi Samueli, Taona, ndidzacita mwa Israyeli coliritsa mwini khutu kwa munthu yense wakucimva.

12. Tsiku lija udidzamcitira Eli zonse ndinaneneratu za pa banja lace, kuciyamba ndi kucitsiriza.

13. Popeza ndinamuuza kuti ndidzaweruza nyumba yace kosatha cifukwa ca zoipa anazidziwa, popeza ana ace anadzitengera temberero, koma iye sanawaletsa.

14. Cifukwa cace ndinalumbira kwa banja la Eli, kuti zoipa za banja la Elilo sizidzafafanizidwa ndi nsembe, kapena ndi zopereka, ku nthawi zonse.

15. Ndipo Samueli anagona kufikira m'mawa, natsegula zitseko za nyumba ya Yehova. Ndipo Samueli anaopa kudziwitsa Eli masomphenyawo.

16. Pamenepo Eli anaitana Samueli, nati, Mwana wanga, Samueli. Nati iye, Ndine.

17. Ndipo anati, Anakuuza cinthu canji? Usandibisire ine. Mulungu akulangendi kuonjezapo, ngati undibisira cimodzi ca zonse zija adanena nawe.

18. Ndipo Samueli anamuuza zonse, sanambisira kanthu. Ndipo iye anati, Ndiye Yehova; acite comkomera pamaso pace.

19. Ndipo Samueli anakula, Yehova nakhala naye, osalola kuti mau ace amodzi apite pacabe.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 3