Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 3:7-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Koma Samueli sanadziwe Yehova, ndiponso mau a Yehova sanaululidwe kwa iye.

8. Ndipo Yehova anabwereza kumuitana Samueli nthawi yacitatu. Ndipo iye anauka napita kwa Eli, nati, Ndine, pakuti mwandiitana ndithu. Ndipo Eli anazindikira kuti ndiye Yehova amene analikuitana mwanayo.

9. Cifukwa cace Eli anati kwa Samueli, Pita, ukagone; ndipo akakuitananso, ukabvomere, kuti, Nenani, Yehova, popeza mnyamata wanu akumva. Comweco Samueli anakagona m'malo mwace.

10. Ndipo Yehova anabwera, naimapo, namuitana monga momwemo, Samueli, Samueli. Pompo Samueli anayankha, Nenani, popeza mnyamata wanu akumva.

11. Ndipo Yehova ananena ndi Samueli, Taona, ndidzacita mwa Israyeli coliritsa mwini khutu kwa munthu yense wakucimva.

12. Tsiku lija udidzamcitira Eli zonse ndinaneneratu za pa banja lace, kuciyamba ndi kucitsiriza.

13. Popeza ndinamuuza kuti ndidzaweruza nyumba yace kosatha cifukwa ca zoipa anazidziwa, popeza ana ace anadzitengera temberero, koma iye sanawaletsa.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 3