Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 20:32-43 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

32. Ndipo Jonatani anayankha Sauli atate wace, nanena, Aphedwe cifukwa ninji? anacitanji?

33. Ndipo Sauli anamponyera mkondo kuti amgwaze; momwemo Jonatani anazindikira kuti atate wace anatsimikiza mtima kupha Davide.

34. Pamenepo Jonatani anauka pagome wolunda ndithu, osadya kanthu tsiku laciwiri la mwezi, pakuti mtima wace unali ndi cisoni cifukwa ca Davide, popeza atate wace anamcititsa manyazi.

35. Ndipo m'mawa, Jonatani ananka kuthengoko pa nthawi imene anapangana ndi Davide, ali ndi kamnayamata.

36. Ndipo anauza mnyamata waceyo, Thamanga uzikatola mibvi Imene ndidzaponya; ndipo analikuthamanga mnyamatayu, iye anaponya mubvi kuutumphitsa iye.

37. Ndipo mnyamatayo atafika pa malo a mubvi umene Jonatani anauponya, Jonatani anapfuulira mnyamatayo, nati, Mubviwo suli m'tsogolo mwako kodi?

38. Ndipo Jonatani anapfuulira mnyamatayo, nati, Yendesa, fulumira, usaima. Ndi mnyamata wa Jonatani anatola mibvi, nafika kwa mbuye wace.

39. Koma mnyamatayo sanadziwa kanthu; Davide ndi Jonatani okha anadziwa za mranduwoo.

40. Ndipo Jonatani anapatsa mnyamata wace zida zace, nanena naye, Muka, tenga izi kunka nazo kumudzi.

41. Pomwepo pocoka mnyamatayo, Davide anauka cakumwera, nagwa nkhope yace pansi, nawerama katatu; ndipo iwowa anapsompsonana, nalirirana, kufikira Davide analiritsa.

42. Ndipo Jonatani ananena kwa Davide, Muka mumtendere, popeza tonsefe tinalumbira m'dzina la Yehova, kuti, Yehova adzakhala pakati pa ine ndi iwe, ndi pakati pa mbeu yanga ndi mbeu yako, nthawi zamuyaya.

43. Ndipo iye ananyamuka nacoka; koma Jonatani anamuka kumudzi.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 20