Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 20:16-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Comweco Jonatani anapangana pangano ndi nyumba ya Davide, ndipo Yehova anakwaniritsa izi polanga adani a Davide.

17. Ndipo Jonatani anamlumbiritsa Davide kaciwiri, cifukwa anamkonda; popeza anamkonda monga anakonda moyo wa iye yekha.

18. Tsono Jonatani ananena kwa Davide, Mawa mwezi ukhala; ndipo adzakufuna, popeza udzasoweka pamalo pako.

19. Ndipo atapita masiku atatu, utsike msanga, nufike kumene unabisala tsiku la mrandu uja, nukhale pa mwala wa Ezeri.

20. Ndipo ine ndidzaponya mibvi itatu pambali pace, monga ngati ndirikuponya pacandamali.

21. Ndipo taona, ndidzatumiza mnyamatayo, ndi kuti, Kafune mibviyo, Ndikamuuza mwanayo, kuti, Taona mibvi iri cakuno; uitole nubwere, popeza pali mtendere kwa iwe, palibe kanthu, pali Yehova.

22. Koma ndikati kwa mnyamatayo, Ona mibvi iri kutsogoloko; pamenepo unyamuke ulendo wako; popeza Yehova wakuuza umuke.

23. Ndipo za cija tinakambirana iwe ndi ine, taona, Yehova ali pakati pa ife nthawi zonse.

24. Comweco Davide anabisala kuthengo; ndipo pakukhala mwezi, mfumu inakhala pansi kudya.

25. Mfumu nikhala pa mpando wace, monga adafocita nthawi zina, pa mpando wa pafupi pa khoma. Ndipo Jonatani anaimirira, ndi Abineri anakhala pa mbali ya Sauli; koma Davide anasoweka pamalo pace.

26. Koma Sauli sananena kanthu tsiku lomwelo; cifukwa anaganizira, Kanthu kanamgwera iye, ali wodetsedwa; indedi ali wodetsedwa.

27. Ndipo kunali tsiku laciwiri mwezi utakhala, Davide adasowekanso pamalo pace; ndipo Sauli anati kwa Jonatani mwana wace, Mwana wa Jese walekeranji kubwera kudya dzulo ndi lero lomwe?

28. Ndipo Jonatani anayankha Sauli, Davide anandiumiriza ndimlole amuke ku Betelehemu;

29. nati, Ndiloleni, ndimuke; cifukwa banja lathu lipereka nsembe m'mudzimo; ndi mbale wanga anandiuzitsa ndifikeko; tsono ngati wandikomera mtima undilole ndicoke, ndikaone abale anga. Cifukwa ca ici safika ku gome la mfumu.

30. Pamenepo Sauli anapsa mtima ndi Jonatani, nanena naye, Iwe mwana wa mkazi wa matsutso ndi wopikisana, sindidziwa kodi kuti wasankha mwana wa Jeseyo kudzinyaza wekha, ndi usiwa wa mai wako yemwe?

31. Popeza nthawi yonse mwana wa Jeseyo akhala ndi moyo padziko, koma sudzakhazikika iwe, kapena ufumu wako. Cifukwa cace tumiza tsopano numtengere kuno kwa ine, popeza adzafa ndithu,

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 20