Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 2:12-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Koma ana a Eli anali oipa; sanadziwa Yehova.

13. Ndipo macitidwe a ansembe akucitira anthu ndiwo, kuti pamene munthu ali yense akapereka nsembe, mnyamata wa wansembeyo akabwera, nyama iri ciwirire, ndi cobvuulira ca ngowe ca mana atatu m'dzanja lace;

14. nacipisa m'cimphuli, kapena mumkhate, kapena m'nkhali, kapena mumphika; yonse imene cobvuuliraco cinaiturutsa, wansembeyo anaitenga ikhale yace. Adafotero ku Silo ndi Aisrayeli onse akufika kumeneko.

15. Ngakhale asanayambe kupsereza mafuta, amadza mnyamata wa wansembe, namuuza wopereka nsembe, nati, Umpatse wansembeyo nyama yoti akaoce; pakuti safuna nyama yako yophika koma yaiwisi.

16. Ndipo ngati munthu akanena naye, Koma adzatentha mafuta tsopano apa, atatha, utenge monga mtima wako ufuna; uyo akanena naye, lai, koma undipatsire iyo tsopanoli, ukapanda kutero ndidzailanda.

17. Ndipo zoipa za anyamatawo zinali zazikuru ndithu pamaso pa Yehova; pakuti anthu anaipidwa ndi nsembe ya Yehova.

18. Koma Samueli anatumikira pamaso pa Yehova akali mwana, atamangira m'cuuno ndi efodi wabafuta.

19. Ndiponso amace akamsokera mwinjiro waung'ono, nabwera nao kwa iye caka ndi caka, pakudza pamodzi ndi mwamuna wace kudzapereka nsembe ya pacaka.

20. Ndipo Eli anadalitsa Elikana ndi mkazi wace, nati, Yehova akupatse mbeu ndi mkazi uyu m'malo mwa iye amene munampempha kwa Yehova. Ndipo iwowa anabwera kwao.

21. Ndipo Yehova anakumbukila Hana, naima iye, nabala ana amuna atatu, ndi ana akazi awiri. Ndipo mwanayo Samueli anakula pamaso pa Yehova.

22. Ndipo Eli anali wokalamba ndithu; namva zonse ana ace anacitira Aisrayeli onse, ndi kuti anagona ndi akazi akusonkhana pa khomo la cihema cokomanako.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 2