Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 18:9-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndipo kuyambira tsiku lomwelo ndi m'tsogolo mwace, Sauli anakhala maso pa Davide.

10. Ndipo kunali m'mawa mwace, mzimu woipa wocokera kwa Mulungu unamgwira Sauli mwamphamvu, iye nalankhula moyaruka m'nyumba yace; koma Davide anayimba ndi dzanja lace, monga amacita tsiku ndi tsiku; koma m'dzanja la Sauli munali mkondo.

11. Ndipo Sauli anaponya mkondowo; pakuti anati, Ndidzapyoza Davide ndi kumphatikiza ndi khoma. Ndipo Davide analewa kawiri kucoka pamaso pace.

12. Ndipo Sauli anaopa Davide, cifukwa Yehova anali naye, koma adamcokera Sauli.

13. Cifukwa cace Sauli anamcotsa kuti asakhale naye, namuika akhale mtsogoleri wace wa anthu cikwi cimodzi; ndipo iye anatsogolera anthu kuturuka ndi kubwera nao.

14. Ndipo Davide anakhala wocenjera m'mayendedwe ace onse; ndipo Yehova anali naye.

15. Ndipo pamene Sauli anaona kuti analikukhala wocenjera ndithu anamuopa.

16. Koma Aisrayeli onse ndi Ayuda onse anamkonda Davide pakuti anawatsogolera kuturuka ndi kulowa nao.

17. Ndipo Sauli anati kwa Davide, Ona, mwana wanga wamkazi wamkuru, dzina lace Merabi, iyeyo ndidzakupatsa akhale mkazi wako; koma undikhalire ngwazi, nuponye nkhondo za Yehova. Pakuti Sauli anati, Dzanja langa lisamkhudze, koma dzanja la Afilisti ndilo.

18. Ndipo Davide anati kwa Sauli, Ine ndine yani, ndi moyo wanga uli wotani, kapena banja la atate wanga liri lotani m'Israyeli, kuti ine ndidzakhala mkamwini wa mfumu?

19. Koma kunali nthawi imene akadapatsa Merabi mwana wamkazi wa Sauli kwa Davide, iye anapatsidwa kwa Adrieli Mholati kukhala mkazi wace.

20. Ndipo Mikala mwana wamkazi wa Sauli anakonda Davide; ndipo pakumva Sauli, anakondwera nako.

21. Nati Sauli, Ndidzampatsa iye, kuti amkhalire msampha, ndi kuti dzanja la Afilisti limgwere. Cifukwa cace Sauli ananena ndi Davide, Lero udzakhala mkamwini wanga kaciwiri.

22. Ndipo Sauli analamulira anyamata ace, nati, Mulankhule naye Davide m'tseri, ndi kuti, Taonani mfumu akondwera nanu, ndi anyamata ace onse akukondani; cifukwa cace tsono, khalani mkamwini wa mfumu.

23. Ndipo anyamata a Sauli analankhula mau awa m'makutu a Davide. Nati Davide, Kodi muciyesera cinthu copepuka kukhala mkamwini wa mfumu, popeza ndiri munthu wosauka, ndi wopeputsidwa.

24. Ndipo anyamata a Sauli anamuuza, kuti, Anatero Davide.

25. Nati Sauli, Mudzatero kwa Davide, kuti mfumu safuna colowolera cina, koma nsonga za makungu zana limodzi za Afilisti, kuti abwezere cilango adani a mfumu. Koma Sauli anaganizira kupha Davide ndi dzanja la Afilisti.

26. Ndipo pamene anyamata ace anauza Davide mau awa, kudamkomera Davide kukhala mkamwini wa mfumu.

27. Ndipo asanathe masikuwo, ananyamuka Davide, ndi anthu ace, nakaphako Afilisti mazana awiri, ndipo Davide anatenga nsonga za makungu ao nazipatsa mofikira kwa mfumu, kuti akhale mkamwini wa mfumu. Ndipo Sauli anampatsa Mikala mwana wace wamkazi akhale mkazi wace.

28. Ndipo Sauli anaona, nadziwa kuti Yehova ali ndi Davide; ndi kuti Mikala mwana wa Sauli anamkonda Davide.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 18