Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 18:1-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunali, pakutsiriza iye kulankhula ndi Sauli, mtima wa Jonatani unalumikizika ndi mtima wa Davide, ndipo Jonatani anamkonda iye monga moyo wa iye yekha.

2. Ndipo Sauli anamtenga tsiku lomwelo, osamlolanso apite kwao kwa atate wace.

3. Pamenepo Jonatani ndi Davide anapangana pangano, pakuti adamkonda iye ngati moyo wa iye yekha.

4. Ndipo Jonatani anabvula maraya ace anali nao, napatsa Davide, ndi zobvala zace, ngakhale lupanga lace, ndi uta wace, ndi lamba lace.

5. Ndipo Davide anaturuka kunka kuli konse Sauli anamtumako, nakhala wocenjera; ndipo Sauli anamuika akhale woyang'anira anthu a nkhondo; ndipo ici cinakomera anthu onse, ndi anyamata a Sauli omwe.

6. Ndipo kunali pakudza iwo, pamene Davide anabwera atapha Afilistiwo, anthu akazi anaturuka m'midzi yonse ya Israyeli, ndi kuyimba ndi kubvina, kuti akakomane ndi mfumu Sauli, ndi malingaka, ndi cimwemwe, ndi zoyimbira.

7. Ndipo akazi anathirirana mang'ombe m'kuyimba kwao, nati,Sauli anapha zikwi zace,Koma Davide zikwi zace zankhani.

8. Koma Sauli anakwiya ndithu, ndi kunenaku kunamuipira; nati, Kwa Davide anawereogera zikwi zankhani, koma kwa ine zikwi zokha; cimperewera ncianioso, koma ufumu wokha?

9. Ndipo kuyambira tsiku lomwelo ndi m'tsogolo mwace, Sauli anakhala maso pa Davide.

10. Ndipo kunali m'mawa mwace, mzimu woipa wocokera kwa Mulungu unamgwira Sauli mwamphamvu, iye nalankhula moyaruka m'nyumba yace; koma Davide anayimba ndi dzanja lace, monga amacita tsiku ndi tsiku; koma m'dzanja la Sauli munali mkondo.

11. Ndipo Sauli anaponya mkondowo; pakuti anati, Ndidzapyoza Davide ndi kumphatikiza ndi khoma. Ndipo Davide analewa kawiri kucoka pamaso pace.

12. Ndipo Sauli anaopa Davide, cifukwa Yehova anali naye, koma adamcokera Sauli.

13. Cifukwa cace Sauli anamcotsa kuti asakhale naye, namuika akhale mtsogoleri wace wa anthu cikwi cimodzi; ndipo iye anatsogolera anthu kuturuka ndi kubwera nao.

14. Ndipo Davide anakhala wocenjera m'mayendedwe ace onse; ndipo Yehova anali naye.

15. Ndipo pamene Sauli anaona kuti analikukhala wocenjera ndithu anamuopa.

16. Koma Aisrayeli onse ndi Ayuda onse anamkonda Davide pakuti anawatsogolera kuturuka ndi kulowa nao.

17. Ndipo Sauli anati kwa Davide, Ona, mwana wanga wamkazi wamkuru, dzina lace Merabi, iyeyo ndidzakupatsa akhale mkazi wako; koma undikhalire ngwazi, nuponye nkhondo za Yehova. Pakuti Sauli anati, Dzanja langa lisamkhudze, koma dzanja la Afilisti ndilo.

18. Ndipo Davide anati kwa Sauli, Ine ndine yani, ndi moyo wanga uli wotani, kapena banja la atate wanga liri lotani m'Israyeli, kuti ine ndidzakhala mkamwini wa mfumu?

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 18