Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 17:37-44 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

37. Nati Davide, Yehova wakundipulumutsa pa mphamvu ya mkango, ndi mphamvu ya cimbalangondo, Iyeyu adzandipulumutsa m'dzanja la Mfilisti uyu, Ndipo Sauli anati kwa Davide, Muka, Yehova akhale nawe.

38. Ndipo Sauli anabveka Davide zobvala zace za iye yekha, nambveka cisoti camkuwa pamutu pace, nambvekanso maraya aunyolo.

39. Ndipo Davide anamanga lupanga lace pamwamba pa zobvala zace, nayesa kuyenda nazo; popeza sanaziyesera kale. Ndipo Davide anati kwa Sauli, Sindikhoza kuyenda ndi izi; pakuti sindinazizolowera. Nazibvula Davide.

40. Natenga ndodo yace m'dzanja lace nadzisankhira miyala isanu yosalala ya mumtsinje, naiika m'thumba la kubusa, limene anali nalo ndilo cibete; ndi coponyera miyala cinali m'dzanja lace, momwemo anayandikira kwa Mfilistiyo.

41. Ndipo Mfilistiyo anadza, nayandikira kwa Davide; ndi wonyamula cikopa cace anamtsogolera.

42. Ndipo Mfilisti pakumwazamwaza maso, ndi kuona Davide, anampeputsa; popeza anali mnyamata cabe, wofiirira, ndi wa nkhope yokongola.

43. Ndipo Mfilisti anati kwa Davide, Ine ndine garu kodi, kuti iwe ukudza kwa ine ndi ndodo? Ndi Mfilistiyo anatukwana Davide nachula milungu yace.

44. Ndipo Mfilistiyo anati kwa Davide, Idza kuno kwa ine, ndidzapatsa mnofu wako kwa mbalame za mlengalenga, ndi kwa zirombo za kuthengo.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 17