Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 17:25-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Nati Aisrayeli, Kodi mwaona munthu uyu amene anakwera kuno? zoonadi iye anakwera kuti adzanyoze Israyeli, ndipo munthu wakumupha iye, mfumu idzamlemeza ndi cuma cambiri, nidzampatsa mwana wace wamkazi, nidzayesa nyumba ya atate wace yaufulu m'Israyeli.

26. Ndipo Davide analankhula ndi anthu akuima pafupi ndi iye, nati, Adzamcitira ciani munthu wakupha Mfilisti uyu, ndi kucotsa tonzo lace pakati pa Israyeli? pakuti Mfilisti uyu wosadulidwa ndiye yani, kuti azinyoza makamu a Mulungu wamoyo?

27. Ndipo anthuwo anamyankha motero, nati, Adzamcitira munthu wakumupha iye mwakuti mwakuti.

28. Ndipo Eliabu mkuru wace anamumva iye alikulankhula ndi anthu; ndipo Eliabu anapsa mtima ndi Davide, nati, Unatsikiranji kuno? ndi nkhosa zija zowerengeka unazisiya ndi yani, m'cipululu muja? Ine ndidziwa kudzikuza kwako ndi kuipa kwa mtima wako; pakuti watsika kuti udzaone nkhondoyi.

29. Ndipo Davide anati, Ndacitanji tsopano? Palibe cifukwa kodi?

30. Napotolokera iye kwa munthu wina, nalankhula mau omwewo; ndipo anthu anamyankhanso monga momwemo.

31. Ndipo pamene mau adanena Davide anamveka, anawapitiriza kwa Sauli; ndipo iye anamuitana.

32. Ndipo Davide anati kwa Sauli, Asade nkhawa munthu ali yense cifukwa ca iyeyo; ine kapolo wanu ndidzapita kuponyana ndi Mfilisti uyu.

33. Ndipo Sauli anati kwa Davide, Sukhoza iwe kukomana ndi Mfilisti uyu kukaponyana naye; pakuti iwe ndiwe mnyamata, koma iye anazolowera nkhondo kuyambira ubwana wace.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 17