Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 17:1-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamenepo Afilisti anasonkhanitsa makamu ao a nkhondo, naunjikana ku Soko wa ku Yuda, namanga zithando pakati pa Soko ndi Azeka ku Efesi-damimu.

2. Ndipo Sauli ndi anthu a Israyeli anasonkhana, namanga zithando pa cigwa ca Ela, nandandalitsa nkhondo yao kuti akaponyane ndi Afilisti.

3. Ndipo Afilisti anaima paphiri tsidya lija, ndi Aisrayeli anaima paphiri tsidya lina; ndi pakati pao panali cigwa.

4. Ndipo ku zithando za Afilisti kunaturuka ciwinda, dzina lace Goliate wa ku Gati, kutalika kwace ndiko mikono isanu ndi umodzi ndi cikhato.

5. Ndipo anali ndi cisoti camkuwa pamutu pace, nabvala maraya aunyolo, olemera ngati masekeli zikwi zisanu za mkuwa,

6. nakuta msongolo wace ndi cobvala camkuwa, ndiponso pacikota pace panali nthungo yamkuwa.

7. Ndipo mtengo wa mkondo wace unali ngati mtanda woombera nsaru; ndi khali la mkondowo linalemera ngati masekeli mazana asanu ndi limodzi a citsulo; ndipo womnyamulira cikopa anamtsogolera.

8. Naima iye naitana makamu a nkhondo a Israyeli, nanena nao, Munaturukiranji kundandalitsa nkhondo yanu? Sindine Mfilisti kodi, ndi inu anyamata a Sauli? mudzisankhire munthu, atsikire kwa ine.

9. Akakhoza iyeyo kuponyana ndi ine ndi kundipha, tidzakhala ife akapolo anu; koma ine ndikamlaka, ndi kumupha, tsono mudzakhala inu akapolo athu, ndi kutitumikira ife.

10. Nati Mfilistiyo, Ine ndinyoza makamu a nkhondo a Israyeli lero; mundipatse munthu, kuti tilimbane ife awiri.

11. Ndipo pamene Sauli ndi Aisrayeli onse anamva mau ao a Mfilistiyo, anadodoma, naopa kwambiri.

12. Tsono Davide anali mwana wa M-efrati uja wa ku Betelehemu-Yuda, dzina lace ndiye Jese; ameneyu anali nao ana amuna asanu ndi atatu; ndipo m'masiku a Sauli munthuyo anali nkhalamba, mwa anthu.

13. Ndipo ana atatu akuru a Jese anatsata Sauli kunkhondoko; ndi maina ao a ana ace atatuwo adapita ku nkhondowo ndiwo Eliabu woyambayo, ndi mnzace womponda pamutu pace Abinadabu, ndi wacitatu Sama.

14. Ndipo Davide anali wotsiriza; ndi akuru atatuwo anamtsata Sauli.

15. Koma Davide akamuka kwa Sauli, nabwerera kudzadyetsa nkhosa za atate wace ku Betelehemu.

16. Ndipo Mfilistiyo anayandikira m'mawa ndi madzulo, nadzionetsera masiku makumi anai.

17. Ndipo Jese anati kwa Davide mwana wace, Uwatengere abale ako efa watirigu uyu wokazinga, ndi mikate iyi khumi, nuthamangire nazo kuzithando kwa abale ako;

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 17