Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 14:41-52 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

41. Cifukwa cace Sauli ananena ndi Yehova, Mulungu wa Israyeli, muonetse coonadi. Ndipo maere anagwera Sauli ndi Jonatani; koma anthuwo anapulumuka.

42. Ndipo Sauli anati, Mucite maere pakati pa ine ndi Jonatani mwana wanga. Ndipo anagwera Jonatani.

43. Pamenepo Sauli ananena ndi Jonatani, Undiuze cimene unacita. Ndipo Jonatani anamuuza, nati, Zoonadi ndinangolawako uci pang'ono ndi nsonga ya ndodo inali m'dzanja langa: ndipo onani ndiyenera kufa.

44. Pamenepo Sauli anati, Mulungu andilange, naoniezereko, pakuti udzafa ndithu, Jonatani.

45. Ndipo anthuwo ananena ndi Sauli, Kodi Jonatani adzafa, amene anacititsa cipulumutso cacikuru ici m'Israyeli? Musatero. Pali Yehova, palibe tsitsi limodzi la pa mutu wace lidzagwa pansi, pakuti iye anagwirizana ndi Mulungu lero. Comweco anthuwo anapulumutsa Jonatani kuti angafe. Ndipo Sauli analeka kuwapitikitsa Afilistiwo;

46. ndi Afilistiwo anamuka ku malo a iwo okha.

47. Ndipo pamene Sauli atakhazikitsa ufumu wa pa Israyeli, iye anaponyana ndi adani ace onse pozungulira ponse, ndi Moabu, ndi ana a Amoni, ndi Edomu ndi mafumu a Zoba, ndi Afilisti; ndipo pali ponse anapotolokerapo, anawalanga.

48. Ndipo iye anakula mphamvu, nakantha Aamaleki, napulumutsa Aisrayeli m'manja a akuwawawanya.

49. Ndipo ana a Sauli ndiwo Jonatani, ndi Isivi, ndi Malikisuwa; ndi maina a ana akazi ace awm ndi awa: dzina la woyamba ndiye Merabu, ndi dzina la mng'ono wace ndiye Mikala;

50. ndi dzina la mkazi wa Sauli ndi Ahinamu mwana wa Ahimazi; ndi dzina la kazembe wa khamu lankhondo lace ndiye Abineri mwana wa Neri, mbale wace wa atate wa Sauli.

51. Ndipo atate wa Sauli ndiye Kisi; ndipo Neri atate wa Abineri ndiye mwana wa Abiyeli.

52. Ndipo panali nkhondo yowawa ndi Afilisti masiku onse a Sauli; ndipo Sauli pakuona munthu wamphamvu, kapena ngwazi, anamtenga akhale naye.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 14