ndi dzina la mkazi wa Sauli ndi Ahinamu mwana wa Ahimazi; ndi dzina la kazembe wa khamu lankhondo lace ndiye Abineri mwana wa Neri, mbale wace wa atate wa Sauli.