Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 14:13-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ndipo Jonatani anakwera cokwawa, ndi wonyamula zida zace anamtsata; ndi Afilisti anagwa pamaso pa Jonatani, ndi wonyamula zida zace anawapha pambuyo pace.

14. Kuwapha koyambako, Jonatani ndi wonyamula zida zace, anapha monga anthu makumi awiri, monga ndime ya munda yolima ng'ombe ziwiri tsiku limodzi.

15. Ndipo kunali kunthunthumira kuzithando, kuthengoko, ndi pakati pa anthu onse; a ku kaboma ndi owawanya omwe ananthunthumira; ndi dziko linagwedezeka; comweco kunali kunthunthumira kwakukuru koposa,

16. Ndipo ozonda a Sauli ku Gibeya wa ku Benjamini anayang'ana; ndipo, onani, khamu la anthu linamwazikana, kulowa kwina ndi kwina.

17. Pamenepo Sauli ananena ndi anthu amene anali naye, Awerenge tsopano, kuti tizindikire anaticokera ndani. Ndipo pamene anawerenga, onani Jonatani ndi wonyamula zida zace panalibe.

18. Ndipo Sauli ananena ndi Ahiya, Bwera nalo likasa la Mulungu kuno. Pakuti likasa la Mulungu linali kumeneko masiku aja ndi ana a Israyeli.

19. Ndipo kunali m'mene Sauli anali cilankhulire ndi wansembeyo, phokoso la m'cigono ca Afilisti linacitikabe, nilikula; ndipo Sauli ananena ndi wansembeyo, Bweza dzanja lako.

20. Ndipo Sauli ndi anthu onse amene anali naye anaunjikana pamodzi, naturukira kunkhondoko; ndipo taonani, munthu yense anakantha mnzace ndi lupanga, ndipo panali kusokonezeka kwakukuru.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 14