Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 10:10-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndipo pamene anafika kucitunda kuja, onani, gulu la aneneri linakomana naye; ndi Mzimu wa Mulungu unamgwera mwamphamvu, iye nanenera pakati pao,

11. Ndipo kunali, kuti onse amene anamdziwiratu kale, pakuona ici cakuti, onani, iye ananenera pamodzi ndi aneneri, anati wina ndi mnzace, Ici nciani cinamgwera mwana wa Kisi? Kodi Saulinso ali mwa aneneri?

12. Ndipo munthu wina wa komweko anayankha nati, Ndipo atate wao ndiye yani? Cifukwa cace mauwa anakhala ngati mwambi, Kodi Saulinso ali mwa aneneri?

13. Ndipo pamene adatha kunenera anafika kumsanjeko.

14. Ndipo mbale wa atate wace wa Sauli ananena kwa iye ndi mnyamata wace, Munanka kuti? Ndipo iye anati, Kukafuna aburuwo; ndipo pakuona kuti sitinawapeza, tinadza kwa Samueli.

15. Ndipo mbale wa atate wa Sauli anati, Undiuze cimene Samueli analankhula nawe.

16. Ndipo Sauli anati kwa mbale wa atate wace, Anatiuza momveka kuti aburuwo anapezedwa kale. Koma sanamdziwitsa mau aja Samueli ananena zaufumuwo.

17. Ndipo Samueli anaitana anthu onse asonkhane kwa Yehova ku Mizipa;

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 10