Ndipo pamene anafika kucitunda kuja, onani, gulu la aneneri linakomana naye; ndi Mzimu wa Mulungu unamgwera mwamphamvu, iye nanenera pakati pao,