Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 9:17-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Ndipo Solomo anamanganso Gezeri, ndi Betihoroni wakunsi,

18. ndi Balati, ndi Tadimori wa m'cipululu m'dziko muja,

19. ndi midzi yonse yosungamo zinthu zace za Solomo, ndi midzi yosungamo magareta ace, ndi midzi yokhalamo apakavalo ace, ndi zina ziti zonse zidakomera Solomo kuzimanga m'Yerusalemu, ndi ku Lebano, ndi m'dziko lonse la ufumu wace.

20. Ndipo Aamori, ndi Ahiti, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi otsala, amene sanali a ana a Israyeli,

21. ana ao amene adatsala m'dziko, amene ana a lsrayeli sanakhoza kuononga konse, Solomo anawasenzetsa msonkho wa nchito kufikira lero.

22. Koma Solomo sanawayesa ana a Israyeli akapolo, koma iwowo anali anthu a nkhondo, ndi anyamata ace, ndi akalonga ace, ndi akazembe ace, ndi oyang'anira magareta ace ndi apakavalo ace.

23. Ameneyo anali akulu a akapitao oyang'anira nchito ya Solomo, mazana asanu mphambu makumi asanu akulamulira anthu ogwira nchito aja.

24. Koma mwana wamkazi wa Farao anaturuka m'mudzi wa Davide kukwera ku nyumba yace adammangira Solomo, pamenepo iye anamanganso Milo.

25. Ndipo caka cimodzi Solomo anapereka katatu nsembe zopsereza ndi zamtendere, pa guwa la nsembe limene anammangira Yehova, nafukiza zonunkhira pa guwa la nsembe pamaso pa Yehova, atatsiriza nyumbayo.

26. Ndipo mfumu Solomo anamanga zombo zambiri ku Ezioni Geberi uli pafupi ndi Eloti, pambali pa Nyanja Yofiira, ku dziko la Edomu.

27. Ndipo, Hiramu anatuma anyamata ace m'zombozo amarinyero ozerewera m'nyanja, pamodzi ndi anyamata a Solomo.

28. Ndipo iwo anafika ku Ofiri, natengako golidi matalenti mazana anai mphambu makumi awiri, nafika naye kwa mfumu Solomo.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 9