Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 8:43-50 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

43. mverani Inu m'Mwamba mokhala Inu, ndipo citani monga mwa zonse mlendoyo azipempha kwa Inu; kuti anthu onse a dziko lapansi adziwe dzina lanu, kuopa Inu, monga amatero anthu anu Aisrayeli, ndi kuti adziwe kuti nyumba yino ndaimangayi yachedwa dzina lanu.

44. Akaturuka anthu anu kukayambana nkhondo ndi adani ao, kumene konse inu mudzawatuma, ndipo akapemphera kwa Yehova molunjika ku mudzi uno munausankha Inu, ndi ku nyumba ndamangira dzina lanu;

45. pamenepo mverani Inu m'Mwamba pempho ndi pembedzero lao, ndi kulimbitsa mlandu wao.

46. Akacimwira Inu, popeza palibe munthu wosacimwa, ndipo mukakwiya nao ndi kuwapereka kwa adani, kuti iwo awatenge ndende kumka nao ku dziko la adani, ngati kutali kapena kufupi,

47. ndipo akakumbukila mitima yao, ali kudziko kumene anatengedwa ukapolo, nakalapa, nakapembedza inu m'dziko la iwo anawatenga ndende, ndi kuti, Tacimwa, ndipo tacita mphulupulu, tacita moipa;

48. ndipo akabwerera kwa Inu ndi mtima wao wonse ndi moyo wao wonse, m'dziko la adani ao adawatenga ndendewo, ndipo akapemphera kwa Inu molunjika ku dziko lao munapatsa makolo aolo, ku mudzi munausankha Inu, ndi kunyumba ndamangira dzina lanu;

49. pamenepo mverani Inu pemphero ndi pembedzero lao m'Mwamba mokhala Inumo, ndi kulimbitsa mlandu wao,

50. ndi kukhululukira anthu anu adacimwira Inu ndi mphulupulu zao zonse adaparamula nazo kwa Inu; ndipo muwacititsire cifundo iwo amene anawagwira ndende, kuti awacitire cifundo;

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 8