Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 8:42-47 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

42. popeza adzamva za dzina lanu lalikuru ndi dzanja lanu lamphamvu ndi mkono wanu wotambasuka; akabwera iyeyo nadzapemphera molunjika ku nyumba yino;

43. mverani Inu m'Mwamba mokhala Inu, ndipo citani monga mwa zonse mlendoyo azipempha kwa Inu; kuti anthu onse a dziko lapansi adziwe dzina lanu, kuopa Inu, monga amatero anthu anu Aisrayeli, ndi kuti adziwe kuti nyumba yino ndaimangayi yachedwa dzina lanu.

44. Akaturuka anthu anu kukayambana nkhondo ndi adani ao, kumene konse inu mudzawatuma, ndipo akapemphera kwa Yehova molunjika ku mudzi uno munausankha Inu, ndi ku nyumba ndamangira dzina lanu;

45. pamenepo mverani Inu m'Mwamba pempho ndi pembedzero lao, ndi kulimbitsa mlandu wao.

46. Akacimwira Inu, popeza palibe munthu wosacimwa, ndipo mukakwiya nao ndi kuwapereka kwa adani, kuti iwo awatenge ndende kumka nao ku dziko la adani, ngati kutali kapena kufupi,

47. ndipo akakumbukila mitima yao, ali kudziko kumene anatengedwa ukapolo, nakalapa, nakapembedza inu m'dziko la iwo anawatenga ndende, ndi kuti, Tacimwa, ndipo tacita mphulupulu, tacita moipa;

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 8