Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 8:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamenepo Solomo anasonkhanitsa akulu a Israyeli, ndi akulu onse a mafuko, akalonga a nyumba za atate a ana a Israyeli, kwa mfumu Solomo m'Yerusalemu, kukatenga likasa la cipangano ca Yehova m'mudzi wa Davide, ndiwo Ziyoni.

2. Ndipo anthu onse a Israyeli anasonkhana kwa mfumu Solomo kukadyereram'mwezi wa Etanimu, ndiwo mwezi wacisanu ndi ciwiri.

3. Ndipo akulu onse a Israyeli anadza, ansembe nanyamula likasa.

4. Ndipo anatenga likasa la Yehova, ndi cihema cokomanako, ndi zipangizo zonse zopatulika, zinali m'cihemamo, inde zimenezi anazitenga ansembe ndi Alevi.

5. Ndipo mfumu Solomo ndi msonkhano wonse wa Israyeli wosonkhana kwa iye anali naye kulikasa, naphera nkhosa ndi ng'ombe za nsembe zosawerengeka ndi zosadziwika, cifukwa ca unyinji wao.

6. Ndipo ansembe analonga likasa la cipangano ca Yehova kumalo kwace, ku monenera mwa nyumba, ku malo opatulikitsa, munsi mwa mapiko a akerubi,

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 8