Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 7:38-51 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

38. Ndipo anapanga mbiya zamphwamphwa khumi zamkuwa; m'mbiya imodziyo munalowamo madzi a mitsuko yaikuru makumi anai, ndipo mbiya iri yonse inali ya mikono inai: pa phaka liri lonse la maphaka aja khumi panakhala mbiya imodzi.

39. Ndipo anaika maphaka asanu ku dzanja lamanja la nyumba, ndi maphaka asanu ku dzanja lamanzere la nyumba; naika thawalelo ku dzanja lamanja la nyumba kum'mawa kupenya kumwera.

40. Ndipo Hiramu anayenga mbiyazo ndi zoolera ndi mbale zowazira. Motero Hiramu anatsiriza kupanga nchito yonse anaicitira mfumu Solomo ya m'nyumba ya Yehova.

41. Nsanamira ziwirizo, ndi mbale za mitu inali pamwamba pa nsanamira ziwirizo, ndi maukonde awiri ophimbira mbale ziwiri za mitu inali pamwamba pa nsanamirazo,

42. ndi makangaza mazana anai a maukonde awiriwo, mizere iwiri ya makangaza a ukonde umodzi kuphimbira mbale ziwiri za mitu inali pa nsanamirazo,

43. ndi maphaka khumiwo ndi mbiya khumi ziri pa maphakawo,

44. ndi thawale limodzilo, ndi ng'ombe khumi mphambu ziwirizo pansi pa thawale;

45. ndi miphikayo, ndi zoolerazo, ndi mbalezo; inde zotengera zonse zimene Hiramu anampangira mfumu Solomo za m'nyumba ya Yehova, zinali za mkuwa wonyezimira.

46. Mfumu inaziyenga pa cidikha ca ku Yordano, m'dothe ladongo, pauti pa Sukoti ndi Zaritani.

47. Ndipo Solomo anazileka zipangizo zonse osaziyesa, popeza zinacuruka ndithu; kulemera kwace kwa mkuwa wonsewo sikunayeseka.

48. Ndipo Solomo anapanga zipangizo zonse za m'nyumba ya Mulungu: guwa la nsembe lagolidi, ndi gome lagolidi loikapo mikate yoonekera;

49. ndi zoikapo nyali za golidi woyengetsa, zisanu ku dzanja lamanja, zisanu kulamanzere, cakuno ca monenera, ndi maluwa ndi nyali ndi mbano zagolidi;

50. ndi zikho, ndi zozimira nyali, ndi mbale, ndi zipande, ndi zopalira mota za golidi woyengetsa, ndi zomangira zitseko zagolidi, za zitseko za cipinda ca m'katimo, malo opatulikitsa, ndiponso za zitseko za nyumba ya Kacisi.

51. Motero nchito zonse zinatsirizika, zimene mfumu Solomo anacitira nyumba ya Yehova. Ndipo Solomo analonga zinthu adazipatula Davide atate wace, ndizo siliva ndi golidi ndi zipangizo zomwe naziika mosungira cuma ca nyumba ya Yehova.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 7