Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 7:26-37 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Ndipo kucindikira kwace kunali ngati m'manja mwa munthu, ndipo mlomo wace unasadamuka ngati mlomo wa comwera, ngati maluwa akakombo, analowamo madzi a mitsuko yaikuru zikwi ziwiri.

27. Ndipo anapanga maphaka khumi amkuwa, m'litali mwace mwa phaka limodzi mikono inai, ndi kupingasa kwace mikono inai, ndi msinkhu wace mikono itatu.

28. Ndipo mapangidwe a maphakawo anali otere: anali nao matsekerezo ao, ndipo matsekerezo anali pakati pa mbano.

29. Ndipo pa matsekerezo a pakati pa mbano panali ngati mikango ndi ng'ombe ndi akerubi, ndi pamwamba pa mbano panali cosanjikirapo; ndipo pansi pa mikango ndi ng'ombe panaphatikizika zotsetseremba zoyangayanga zokoloweka.

30. Ndipo phaka lid lonse linali ndi njinga zamkuwa zinai ndi mitanda yamkuwa, ndipo ngondya zace zinai zinali ndi mapewa; pansi pa thawale panali mapewa oyengeka pa mbali pa zophatikizika zonse.

31. Ndipo pakamwa pace m'katimo pamwamba pa cosanjikira, panayesa mkono umodzi; koma pakamwa pace panali posadamuka, monga mapangidwe ace a cosanjikira, mkono umodzi ndi nusu; ndiponso pakamwa pace panali zolemba ndi matsekerezo ace anali amphwamphwa, si ozunguniza.

32. Ndipo njinga zinai zinali pansi pa matsekerezo, ndi mitanda ya njinga inali m'mphakamo, ndi msinkhu wa njinga imodzi unali mkono umodzi ndi nusu.

33. Ndipo mapangidwe a njinga analingana ndi mapangidwe a njinga za gareta, mitanda yace ndi mkombero wace ndi nthiti zace ndi mtima wace zonsezo zinayengedwa.

34. Ndipo panali ngati mapewa anai pansi pa ngondya zinai za phaka limodzi, mapewawo anali a phaka lomwelo.

35. Ndipo pamwamba pa phaka panali khoma lozunguniza, msinkhu wace nusu ya mkono; ndi pamwamba pa phaka panali mbano zace ndi matsekerezo a phaka lomwelo.

36. Ndipo m'mapanthi mwa mbano zace ndi pa matsekerezo ace analemba ngati akerubi ndi mikango ndi migwalangwa, monga mwa malo ace a zonsezo, ndi zoyangayanga zozungulira.

37. Motero anapanga maphaka khumiwo, anafanana mayengedwe ao muyeso wao ndi maonekedwe ao.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 7