Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 7:17-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Ndipo panali maukonde olukaluka ndi zoyangayanga, zokolana za pa mitu imene inali pamwamba pa nsanamira; zisanu ndi ziwiri za pa mutu wina, ndi zisanu ndi ziwiri za pa mutu unzace.

18. M'mwemo anapanga nsanamira, ndipo panali mizere iwiri yozungulira ukonde umodzi, kukuta ndi makangaza mituyi inali pamwambapo, nacita momwemo ndi mutu winawo.

19. Ndipo mituyi inali pamwamba pa nsanamira za pa likole inali ngati akakombo malembedwe ace, a mikono inai.

20. Ndipo panalinso mitu pamwamba pa nsanamira ziwirizo, pafupi pa mimbayo, inali m'mbali mwace mwa ukondewo; ndipo makangazawo anali mazana awiri, akukhala mizere yozinga nda nda mutu winawo.

21. Ndipo anaimiritsa nsanamirazi pa likole la Kacisi; naimiritsa nsanamira ya ku dzanja lamanja, nacha dzina lace Yakini; naimiritsa nsanamira yakumanzere, nacha dzina lace Boazi.

22. Ndipo pamwamba pa nsanamirazo panali ngati akakombo malembedwe ace; motero anaitsiriza nchito ya nsanamirazo.

23. Ndipo anayenganso thawale lamkuwa, kukamwa kwace kunali kwa mikono khumi, linali lozunguniza, ndi msinkhu wace unali mikono isanu; ndi cingwe ca mikono makumi atatu cinalizungulira.

24. Ndipo m'khosi mwace munali ngati zikho zozinganiza m'mkono umodzi zikho khumi zakuzinganiza thawalelo; zikhozo zinayengedwa m'mizere iwiri poyengedwa thawalelo.

25. Linasanjikika pa ng'ombe khumi mphambu ziwiri, zitatu zinapenya kumpoto, zitatu kumadzulo, zitatu kumwera, zitatu kum'mawa; ndipo thawalelo linakhazikika pamwamba pa izo; ndipo nkholo zao zinayang'anana.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 7