Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 3:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Solomo anapalana ubwenzi ndi Farao mfumu ya Aigupto, natenga mwana wamkazi wa Farao, nadza naye ku mudzi wa Davide, mpaka atamanga nyumba ya iye yekha, ndi nyumba ya Yehova, ndi linga lozinga Yerusalemu.

2. Koma anthu anaphera nsembe pamisanje, popeza panalibe nyumba yomangira dzina la Yehova kufikira masiku omwewo.

3. Ndipo Solomo anakondana ndi Yehova, nayenda m'malemba a Davide atate wace; koma anaphera nsembe nafukiza zonunkhira pamisanje.

4. Ndipo mfumu inapita ku Gibeoni kukaphera nsembe kumeneko; popeza msanje waukuru unali kumeneko, Solomo anapereka nsembe zopsereza cikwi cimodzi pa guwalo la nsembe.

5. Ku Gibeoni Yehova anaonekera Solomo m'kulota usiku, nati Mulungu, Tapempha cimene ndikupatse.

6. Ndipo Solomo anati, Munamcitira mtumiki wanu Davide atate wanga zokoma zazikulu, monga umo anayenda pamaso panu ndi coonadi ndi cilungamo ndi mtima woongoka ndi Inu; ndipo mwamsungira cokoma ici cacikuru kuti mwampatsa mwana kukhala pa mpando wace wacifumu monga lero lino.

7. Ndipo tsopano, Yehova Inu Mulungu wanga, mwalonga ine kapolo wanu ufumu m'malo mwa atate wanga Davide, koma ine ndine kamwana, sindidziwa kuturuka kapena kulowa.

8. Ndipo kapolo wanu ndiri pakati pa anthu anu amene Inu munawasankha, anthu ambirimbiri osawerengeka, kapena kulembeka m'unyinji wao.

9. Patsani tsono kapolo wanu mtima womvera wakuweruza anthu anu; kuti ndizindikire pakati pa zabwino ndi zoipa; pakuti akutha ndani kuweruza anthu anu ambiri amene?

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 3