Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 21:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo zitatha izi, kunaoneka zotere: Naboti wa ku Yezreeli anali ndi munda wamphesa, unali m'Yezreelimo, m'mbali mwa nyumba ya Ahabu mfumu ya ku Samaria.

2. Ndipo Ahabu analankhula ndi Naboti, nati, diloleni Ndipatse munda wako wamphesa ukhale munda wanga wa ndiwo, popeza uli pafupi ndi nyumba yanga; ndipo m'malo mwace ndidzakupatsa munda wamphesa wokoma woposa uwu; kapena kukakukomera ndidzakupatsa ndalama za pa mtengo wace,

3. Ndipo Naboti anati kwa Ahabu, Pali Yehova, ndi pang'ono ponse ai, kuti ndikupatseni colowa ca makolo anga,

4. Ndipo Ahabu analowa m'nyumba mwace wamsunamo ndi wokwiya, cifukwa ca mau amene Naboti wa ku Yezreeli adalankhula naye; popeza adati, Sindikupatsani colowa ca makolo anga. M'mwemo anagona pa kama wace, nayang'ana kumbali, nakana kudya mkate.

5. Koma Yezebeli mkazi wace anadza kwa iye, nati kwa iye, Mucitiranji msunamo, kuti mukana kudya mkate?

6. Nati kwa iye, Popeza ndinalankhula kwa Naboti wa ku Yezreeli, ndinati kwa iye, Undigulitse munda wako ndi ndalama; kapena ukafuna, ndikupatsa munda wina m'malo mwace; kama anandiyankha, Sindikupatsani munda wanga wamphesa.

7. Ndipo Yezebeli mkazi wace anati kwa iye, Kodi mulamulira Aisrayeli tsopano ndinu? Taukani, idyani mkate, ukondwere mtima wanu; munda wa Naboti wa ku Yezreeli ndidzakupatsani ndine.

8. M'mwemo analemba akalata m'dzina la Ahabu nakhomerapo cizindikilo cace, natumiza akalatawo kwa akulu ndi omveka anali m'mudzi mwace, nakhala naye Naboti.

9. Ndipo analemba m'akalata, nati, Lalikirani kuti asale kudya, muike Naboti pooneka ndi anthu;

10. ndipo muike anthu awiri, anthu oipa, pamaso pace, kuti amcitire umboni, ndi kuti, Watemberera Mulungu ndi mfumu; nimumturutse ndi kumponya miyala kumupha.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 21