Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 20:7-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Pamenepo mfumu ya Israyeli anaitana akulu onse a dziko, nati, Tazindikirani inu, penyani kuti-munthu uyu akhumba coipa; popeza anatuma kwa ine kulanda akazi anga, ndi ana anga, ndi siliva, ndi golidi wanga; ndipo sindinamkaniza.

8. Ndipo akulu onse ndi anthu onse anati kwa iye, Musamvere, musabvomereze.

9. Ndipo anati kwa mithenga ya Benihadadi, Kauzeni mbuye wanga mfumu, Zonse munayamba kundituma mtumiki wanu kuzifunsa ndidzacita, koma ici sindingacicite. Nicoka mithengayo, nimbwezera mau.

10. Ndipo Benihadadi anatuma kwa iye, nati, Milungu indilange, nionjezepo, ngati pfumbi la Samaria lidzafikira kudzaza manja a anthu onse akutsata mapazi anga.

11. Ndipo mfumu ya Israyeli anayankha, nati, Kamuuzeni, Wakumanga zida asadzikuze ngati wakubvulayo.

12. Ndipo kunacitika, atamva Benihadadi mau awa, analikumwa nao mafumu m'misasa, ananena ndi anyamata ace, Nikani. Nandandalika pamudzipo.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 20