Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 20:14-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Nati Ahabu, Mwa yam? Nati, Atero Yehova, Mwa anyamata a akalonga a madera. Natinso, Adzayamba kuponya nkhondo ndani? Nati, Iwe.

15. Pamenepo anawerenga anyamata a akalonga a madera, nawapeza mazana awiri mphambu makumi atatu kudza awiri. Pamenepo anawerenganso anthu onse, ndiwo ana a Israyeli onse zikwi zisanu ndi ziwiri.

16. Ndipo amenewo anaturuka usana. Koma Benihadadi analinkumwa naledzera m'misasamo, iye ndi mafumu aja makumi atatu mphambu awiri aja akumthandiza.

17. Ndipo anyamata a akalonga a madera anayamba kuturuka, koma Benihadadi anatuma anthu, iwo nambwezera mau, kuti, M'Samaria mwaturuka anthu.

18. Nati iye, Cinkana aturukira mumtendere, agwireni amoyo; cinkana aturukira m'nkhondo, agwireni amoyo.

19. Tsono anaturuka m'mudzi anyamata a akalonga a madera aja, ndi khamu la nkhondo linawatsata.

20. Ndipo ali yense anapha munthu wace; ndipo Aaramu anathawa, Aisrayeli nawapitikitsa; ndipo Benihadadi mfumu ya Aramu anathawira pa kavalo pamodzi ndi apakavalo.

21. Tsono mfumu ya Israyeli inaturuka, nikantha apakavalo ndi apamagareta, nawapha Aaramuwo maphedwe akuru.

22. Ndipo mneneri uja anayandikira kwa mfumu ya Israyeli, nati kwa iye, Kadzilimbitseni, mudziwe mucenjere ndi cimene mucicita; popeza caka cikudzaci mfumu ya Aramu idzabweranso kulimbana nanu.

23. Ndipo anyamata a mfumu ya Aramu anati kwa iye, Milungu yao nja kumapiri, ndimo m'mene atilakira; koma tikaponyana nao kucidikha, zedi tidzaposa mphamvu.

24. Tsono citani ici, cotsani mafumu aja yense ku malo ace, muike m'malo mwao akazembe.

25. Ndipo mudziwerengere khamu la nkhondo longa khamu lija lidaonongekalo, ndi akavalo onga akavalo aja, ndi magareta monga omwe aja; ndipo tikaponyane nao pacidikha tidzawapambana ndithu. Namvera iye mau ao, natero kumene.

26. Tsono kunacitika, pakufikanso caka Benihadadi anamemeza Aaramu nakwera ku Meld kukaponyana ndi Aisrayeli.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 20