Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 2:25-38 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Ndipo mfumu Solomo anatuma dzanja la Benaya mwana wa Yehoyada, ndipo anamgwera, namwalira iye.

26. Ndipo mfumu inanena ndi Abyatara wansembeyo, Pita ku Anatoti ku minda yako; pakuti wakutidwa ndi imfa; koma sindikupha iwe lero lino, cifukwa unanyamula likasa la Ambuye Yehova pamaso pa Davide atate wanga, ndi popeza unazunzidwa monse umo atate wanga Davide anazunzidwamo.

27. Motero Solomo anacotsa Abyatara asakhalenso wansembe wa Yehova, kuti akakwaniritse mau a Yehova amene aja adalankhula ku Silo za mbumba ya Eli.

28. Ndipo mbiriyi inamfika Yoabu, pakuti Yoabu anapambukira kwa Adoniya, angakhale sanapambukira kwa Abisalomu. Ndipo Yoabu anathawira ku cihema ca Yehova, nagwira nyanga za guwa la nsembe.

29. Ndipo anamuuza mfumu Solomo, kuti, Yoabu wathawira ku cihema ca Yehova; ndipo taonani, wakhala ku guwa la nsembe. Pomwepo Solomo anatuma Benaya mwana wa Yehoyada, nati, Kamkwereo

30. Nafika Benaya ku cihema ca Yehova, nati kwa iye, Mfumu itero, Taturuka. Nati, Iai, koma ndifere pompano. Ndipo Benaya anabweza mau kwa mfumu, nati, Yoabu wanena cakuti, nandiyankha mwakuti mwakuti.

31. Ndipo mfumu inati kwa iye, Cita monga umo wanena iye, numkwere, numuike; kuti undicotsere ine ndi nyumba ya atate wanga mwazi uja Yoabu anaukhetsa wopanda cifukwa.

32. Ndipo Yehova adzambwezera mwazi wace pa mutu wace wa iye yekha, popeza iye anawakantha anthu awiri olungama ndi okoma oposa iye mwini, nawapha ndi lupanga, atate wanga Davide osadziwa, ndiwo Abineri mwana wa Neri kazembe wa khamu la nkhondo la Israyeli, ndi Amasa mwana wa Yeteri kazembe wa khamu la nkhondo la Yuda.

33. Motero mwazi wao udzabweranso pa mutu wace wa Yoabu, ndi pa mutu wa mbumba yace, ku nthawi yamuyaya; koma Davide, ndi mbumba yace, ndi banja lace, ndi mpando wace wacifumu adzakhala ndi mtendere wa Yehova ku nthawi yamuyaya.

34. Pomwepo Benaya mwana wa Yehoyada anakwera namkantha iye, namupha; ndipo anaikidwa m'nyumba yace yace kucipululu.

35. Ndipo mfumu inaika Benaya mwana wa Yehoyada m'malo mwace kutsogolera khamu la nkhondo, ndi mfumu inaika Zadoki wansembe m'malo mwa Abyatara.

36. Ndipo mfumu inatuma munthu kukaitana Simeyi, nati kwa iye, Udzimangire nyumba m'Yerusalemu, nukhale komweko osaturukako kumka kwina konse.

37. Popeza tsiku lomwelo lakuturuka iwe ndi kuoloka mtsinje Kidroni, tadziwa ndithu kuti udzafadi, mwazi wako udzakhala pa mutu wa iwe wekha.

38. Ndipo Simeyi ananena ndi mfumu, Mau awa ndi abwino; monga momwe mwanena mbuye wanga mfumu momwemo ndidzacita kapolo wanu. Ndipo Simeyi anakhala m'Yerusalemu masiku ambiri.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 2