Nafika Benaya ku cihema ca Yehova, nati kwa iye, Mfumu itero, Taturuka. Nati, Iai, koma ndifere pompano. Ndipo Benaya anabweza mau kwa mfumu, nati, Yoabu wanena cakuti, nandiyankha mwakuti mwakuti.