Ndipo kunacitika, zitapita zaka zitatu, kuti akapolo awiri a Simeyi anathawira kwa Akisi mwana wa Maaka mfumu ya Gati. Ndipo anamuuza Simeyi, nati, Taonani, akapolo anu akhala ku Gati.