Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 18:28-41 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. Ndipo anakwezadi mau, nadzitema monga makhalidwe ao ndi mipeni ndi nthungo, kuti mwazi wao unali cucucu.

29. Ndipo kunali, litapendeka dzuwa, ananenera kufikira nthawi ya kupereka nsembe; koma panalibe mau, kapena wobvomereza, kapena wakuwamvera.

30. Pamenepo Eliya ananena ndi anthu onse, Senderani kwa ine; ndipo onse anasendera kwa iye. Iye nakonza guwa la nsembe la Yehova lidagumukalo.

31. Ndipo Eliya anatenga miyala khumi ndi iwiri, monga mwa ciwerengo ca mafuko a ana a Yakobo, amene mau a Yehova adamfikira, kuti, Dzina lako ndi Israyeli.

32. Ndipo ndi miyalayi anamanga guwa la nsembe m'dzina la Yehova, nazunguniza guwalo ndi mcera, ukulu wace ngati kulandira miyeso iwiri ya mbeu kuzinga guwalo.

33. Ndipo anakonza nkhunizo, naduladula ng'ombe, naiika pankhuni. Nati, Dzazani madzi mbiya zinai, muwathire pa nsembe yopsereza ndi pankhuni.

34. Nati, Bwerezaninso kawiri; nabwerezanso. Nati, Bwerezani katatu; nabwereza katatu.

35. Ndipo madzi anayenda pozinga guwa la nsembe, nadzazanso meerawo ndi madzi.

36. Ndipo kunali, nthawi ya kupereka nsembe yamadzulo, Eliya mneneri anasendera, nati, Yehova Mulungu wa Abrahamu ndi Isake ndi Israyeli, lero kudziwike kuti Inu ndinu Mulungu wa Israyeli, ndi ine mtumiki wanu, kuti mwa mau anu ndacita zonsezi.

37. Ndimvereni Yehova, ndimvereni, kuti anthu awa adziwe kuti Inu Yehova ndinu Mulungu, ndi kuti Inu mwabwezanso mitima yao.

38. Pamenepo moto wa Yehova unagwa, nutentha nsembe yopsereza, ndi nkhuni, ndi miyala, ndi pfumbi, numwereretsa madzi anali mumcera.

39. Ndipo anthu onse anaona, nagwa nkhope zao pansi, nati, Yehova ndiye Mulungu, Yehova ndiye Mulungu.

40. Ndipo Eliya anati kwa iwo, Gwirani aneneri a Baala, asapulumuke ndi mmodzi yense. Nawagwira, ndipo Eliya ana pita nao ku mtsinje wa Kisoni, nawapha pamenepo.

41. Ndipo Eliya ananena ndi Ahabu, Nyamukani, idyani, imwani; popeza kumveka mkokomo: wa mvula yambiri.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 18